NKHANI

M’gwilizano wa mabungwe a Multi Consult Africa ndi National Youth On Climate Change wankhazikitsa ntchito yosamala ndi kuteteza chilengdwe kwa Chagunda boma la Salima.

By Alinafe Nyanda.

Achinyamata wochokera m’dera la mfumu yaikulu Kambwiri ku Salima ati ndi wochilimika komaso wothuthumira  pofuna kuthana ndi mchitidwe owotcha Makala omwe wabvuta kwambiri m’dera lawo.

Achinyamatawa alakhula izi lachitatu pa bwalo la zamasewero la Chagunga pamwambo omwe m’gwilizano wa mabungwe a Multi Consult Africa ndi National Youth On Climate Change unakhazikitsa ndondomeko ya ntchito yosamala ndi kuteteza chilengdwe ndi cholinga chofuna kuphuzitsa achinyamata komaso kuwalimbikitsa kuti azitenga nawo gawo pa ulimi wanjuchi ndi bowa muntchito yomwe akuyitcha kuti Conserve with benift m’chingerezi

Wapampando wa gulu la achinyamata la Chagunda Youth Club,Pickson Gwedeza wati ndiwothokonza pa zomwe mgwilizano wa mabungwewa wawachitira pakati pawo poyambitsa ntchitoyi yomwe wati sithandinza kokha kusamala ndi kuteteza chilengedwe kokha komaso ipindulira achinyamata ambiri omwe amangokhala kuti wadzikhala wodzidalira kudzera mu ilimi wa njuchi ndi bowa.

Gwedeza wati masiko ano achinyamata akuyenera kumakangalika ndi kulimbika kwambiri pantchito yosamala chilengedwe adakali anyonga komaso kuwunika ndi kukonza tsogolo lawo kudzera mu ulimi.

 ‘Ifeyo tikuwona kuti tipindula kwambiri ndi kubwera kwa ntchitoyi mudzi mwanthu angakhale kuti ntchitoyi yangoyamba kumene kaamba koti pakadalipano adakatiphuzitsa momwe tingasamalile njuchi kwinaku tikusamalira nkhalango zanthu posadula mitengo mwachisawawa.” Adatero Gwedeza.

Malinga ndi Gwedeza wati chosangalatsa china ndichakuti mgwirizano wamabungwewa walonjenza achinyamata ozungulira dera la Chaguda kuti posachedwapa uwabweretsera mi’ng’oma yomwe adzisungilamo njuchi,zomwe wati ndi chilimbikitso chabwino pakati pawo kaamba koti adzikahala akugwira ntchitoyi ndi chiyembekezo.

Gwedeza watsimikiza kuti angakhale ntchitoyi itati yadzatha mudzi mwawo iwo ngati achinyamata adzayesetsa kugwirana manja ndi adindo wosiyanasiyana boma la Salima kusamala chilengedwe powonetsetsa kuti anthu ambiri kwa Chagunda aphunzira nawo kuchita ulimi wa njuchi ndi bowa.

Ndipo mau ake mkulu woyendetsa ntchitoyi mugwirizano wa mabungwe a Multi Consult Africa komanso Malawi Youth Network On Climate Change Collings Mitochi wati gwilizano wa mabungwewa udaganiza zoyambitsa ntchitoyi kwa mfumu yayikulu Kwambiri itapenza kuti achinyamata ambiri amasowekera upangiri wa mene angagwiritsire ntchito nkhalango zawo kuti azipindula kusiyana ndi mchitidwe owotcha makala.

Mitochi wati ichi ndi chomwe chidapangitsa kuti aganize zoyambitsa ndondomeko ya ntchitoyi kwa Chagunda pofunitsitsa kupereka danga ndi mwayi pakati pa chinyamata kuti azigwiritsa ntchito bwino nkhalango zawo moyenerera.

“Tikugwila ntchito imeneyi mogwilizana ndi boma kudzera ku khosolo ya Salima pamodzi ndi alangizi azankhalango komanso achinyamata akuno powapatsa maphunziro a mene angapangire  ulimi wa Njuchi komanso Bowa wopindulitsa,” adatero Mitochi.

Mitochi  wati pakadalipano achinyamata wokwana 51 awonetsa kale chidwi chofunitsitsa kutenga nawo gawo pa ntchito yosamala ndi kuteteza chilengedwe kamba koti anawapeza kale ali pa zochitika zina zosamala chilengedwe magulu awo koma chomwe amasowekera ndi upangili wa kuya.

Ntchitoyi yomwe ndi yazaka ziwiri cholinga chake ndikufuna kupereka upangiri pakati pa achinyamata woti azitha kupeza zochita kudzera muzithu zomwe alinazo kale pakati pawo monga nkhalango kwinaku akuthandiza boma posamala ndi kuteteza chilengedwe

Pakadalipano ntchitoyi ikugwilidwa maboma a Salima ndi Nkhatabay ndi chithandizo cha ndalama zokwana 10 million kwacha kuchokera ku bungwe la Dau foundation mdziko la Netherlands ndipo ku Salima ntchitoyi ikugwilidwa munkhalano yotchedwa Namwiri yomwe idapanga malire ndi nkhalango yathuma.

Boma la Salima ndi limodzi mwa maboma omwe amakhudzidwa kwambiri ndi bvuto lowononga chilengedwe maka pankhani yowotcha makala yomwe yapangitsa kuti nkhalango zambiri bomali zipululuke ndi kusakazidwa kwambiri.

End.

Comments

0 comments

Show More

Related Articles

Back to top button
%d bloggers like this: