NKHANI

Ofesi yoona za anthu olowa ndikutuluka m’boma la Salima likhwimitsa ntchito zake

Ofesi yoona za anthu olowa ndikutuluka m’boma la Salima yapempha anthu okhala m’bomali kuti akaona anthu amaiko ena atalowa mdziko lino mopanda zowayeneleza kutero azikafotokoza ku maofesi awo ndicholinga chokhwimitsa chitetezo mdziko muno.

Mkulu wa ofesiyi ku Salima Dalitso Kakhongwe wati anthu akuyenera kupewa kusunga anthu olowa mdziko lino popanda chilolezo m’manyumba mwawo komanso kuthandizila anthuwa kulowa mdziko lino popanda chilolezo pakuti akatero adzayankha mlandu poti ndikuphwanya malamuro adziko lino.

“Chomwe anthu akuyenera kudziwa ndi chakuti ofesi yanthu imagwira ntchito payiyokha  ndipo pakapezeka anthu ena akukuwunzani kuti amagwira ntchito monthandizana ndi ife akukunamizani

“Anthuwa akakwatila ndi kukwatiwa  ndi mzika za dziko lino akufunika kukalembetsa ndikukapeza zikalata zokhalira mdziko muno ku ma ofesiwa”Adatero Kakhongwe.

Kakhongwe adachenjezaso anthu amene amakhala akuyenda maulendo opita ku South Africa kuti amakonda kunamizana kuti akhonza kunthandiza azawo kupeza ziphaso zoyendera mwachangu kuti uku nkubelana komaso kupusitsana kamba koti ndi ofesi yawo yokha imene ingawanthandize mwachangu.

Ndipo mau ake mkhalapampando wa khosolo ya boma la Salima Ester Soko wati ndikofunikira kuti zika za dziko lino zizigwira ntchito limodzi ndi ofesiyi pochepetsa mchitidwe wobelana komaso kulowetsa anthu mdziko muno mozemba.

Soko wayamikira ofesiyi boma la Salima polimbikitsa ntchito yowunikira anthu bomali pazamene iyo amagwirira ntchito komaso kuwachenjeza kuti azikhala osamala akakumana ndi zotere.

Boma la Salima ndi limodzi mwa maboma amene anthu ake amakonda kupita kumayiko akunja monga South africa kukagwira ntchito zosiyanasiyana.

Comments

0 comments

Tags
Show More

Related Articles

Back to top button

Log In

Forgot password?

Forgot password?

Enter your account data and we will send you a link to reset your password.

Your password reset link appears to be invalid or expired.

Log in

Privacy Policy

Add to Collection

No Collections

Here you'll find all collections you've created before.

Close
Close
%d bloggers like this: